Genesis 7:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adaononga zamoyo zonse za pa dziko: anthu, nyama, zokwaŵa ndi mbalame. Nowa yekha adapulumuka pamodzi ndi onse amene anali naye m'chombomo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo zinaonongedwa zamoyo zonse zimene zinali pa dziko lapansi, anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndipo zinaonongedwa pa dziko lapansi: anatsala Nowa yekha ndi amene anali pamodzi naye m'chingalawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chamoyo chilichonse pa dziko lapansi chinawonongedwa, kuyambira munthu, nyama, zokwawa ndi mbalame. Nowa yekha ndiye anatsala pamodzi ndi onse amene anali naye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zinaonongedwa zamoyo zimene zonse zinali pa dziko lapansi, anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndipo zinaonongedwa pa dzikolapansi: anatsala Nowayekha ndi amene anali pamodzi naye m'cingalawa.