Genesis 7:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Utengekonso mbalame ziŵiriziŵiri za mtundu uliwonse, magulu asanu ndi aŵiri. Uchite zimenezi pofuna kuti nyama ndi mbalame za mitundu yonse zisungidwe ndi moyo, ndipo kuti zidzaswanenso pa dziko lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso mbalame za kumlengalenga zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yaimuna ndi yaikazi, kuti mbeu ikhale ndi moyo pa dziko lonse lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chimodzimodzinso mbalame, utenge zisanu ndi ziwiri zazimuna ndi zisanu ndi ziwiri zazikazi za mtundu uliwonse kuti mitundu yawo isungike ndi moyo pa dziko lonse lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiposo mbalame za kumlengalenga zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yaimuna ndi yaikazi, kuti mbeu ikhale ndi moyo pa dziko lonse lapansi.