Genesis 7:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakangopita masiku asanu ndi aŵiri, ndidzagwetsa mvula pa dziko lapansi masiku makumi anai, usana ndi usiku, kuti zife zamoyo zonse zimene ndidazipanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti akapita masiku asanu ndi awiri Ine ndidzavumbitsa mvula pa dziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku; ndi zinthu zamoyo zonse zomwe ndazipanga ndidzaziononga pa dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakapita masiku asanu ndi awiri ndidzagwetsa mvula pa dziko lapansi kwa masiku makumi anayi usana ndi usiku ndipo ndidzawononga cha moyo chilichonse chimene ndinachipanga pa dziko lapansi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti akapita masiku asanu ndi awiri Ine ndidzabvumbitsa mvula pa dziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku; ndi zinthu zamoyo zonse zomwe ndazipanga ndidzaziononga pa dziko lapansi,