Genesis 8:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Mulungu adakumbukira Nowa pamodzi ndi nyama zonse zakuthengo ndi zoŵeta zimene zinali naye m'chombomo. Adalamula mphepo kuti iwombe pa dziko lapansi, pomwepo madzi adayamba kutsika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mulungu anakumbukira Nowa ndi zamoyo zonse, ndi nyama zonse zimene zinali pamodzi naye m'chingalawamo; ndipo Mulungu anapititsa mphepo pa dziko lapansi, naphwa madzi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Mulungu anakumbukira Nowa ndi nyama zonse zakuthengo ndi ziweto zimene anali nazo mu chombo. Yehova anatumiza mphepo pa dziko lapansi ndipo madzi anaphwera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mulungu anakumbukira Nowa ndi zamoyo zonse, ndi nyama zonse zimene zinali pamodzi naye m'cingalawamo; ndipo Mulungu anapititsa mphepo pa dziko lapansi, naphwa madzi;