Genesis 8:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Madzulo idabwerako, ndipo Nowa adaona kuti kukamwa kwake kuli tsamba laliŵisi la mtengo wa olivi. Apo Nowa adadziŵa kuti madzi ayamba kuphwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo njiwa inadza kwa iye madzulo; ndipo, taonani, m'kamwa mwake munali tsamba la azitona lothyoledwa: ndipo anadziwa Nowa kuti madzi analimkuphwa pa dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene nkhunda inabwerera madzulo ake, inali itanyamula tsamba laliwisi la mtengo wa olivi. Motero Nowa anadziwa kuti madzi aphwadi pa dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo njiwa inadza kwa iye madzulo; ndipo, taonani, m'kamwa mwace munali tsamba lazitona lotyoledwa: ndipo anadziwa Nowa kuti madzi analimkuphwa pa dziko lapansi.