Genesis 8:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Nowa atadikiranso masiku ena asanu ndi aŵiri, adaitulutsanso nkhunda ija, koma nkhundayo sidabwererenso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo analindanso masiku ena asanu ndi awiri; natulutsa njiwayo: ndipo siinabweranso konse kwa iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anadikira masiku ena asanu ndi awiri ndipo anatumizanso nkhunda ija, koma nthawi imeneyi sinabwererenso kwa iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo analindanso masiku ena asanu ndi awiri; naturutsa njiwayo: ndipo siinabweranso konse kwa iye.