Genesis 8:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nowa ali wa zaka 601, pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, madzi adaphweratu pa dziko lapansi. Nowa adatsekula zenera la chombo chija nayang'ana kunja, nkuwona kuti pansi pauma,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali chaka cha mazana asanu ndi limodzi kudza chimodzi, mwezi woyamba, tsiku loyamba mwezi, madzi anaphwa pa dziko lapansi; ndipo Nowa anachotsa chindwi lake pachingalawa, nayang'ana, ndipo taonani, padauma pa dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba wa chaka chimene Nowa anakwanitsa zaka 601, madzi anawuma pa dziko lapansi. Ndipo Nowa anachotsa denga la chombo ndipo anaona kuti kunja kwawuma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali caka ca mazana asanu ndi limodzi kudza cimodzi, mwezi woyamba, tsiku loyamba mwezi, madzi anaphwa pa dziko lapansi; ndipo Nowa anacotsa cindwi lace pacingalawa, nayang'ana, ndipo taonani, padauma pa dziko lapansi.