Genesis 8:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta atamva fungo lokomalo, adati, “Sindidzatembereranso dziko chifukwa cha zochita za anthu, chifukwa ndikudziŵa maganizo a munthu kuti ndi oipa kuyambira ali mwana. Sindidzaononganso zamoyo zonse monga ndachitiramu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anamva chonunkhira chakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwake, Sindidzatembereranso konse nthaka chifukwa cha munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndachitiramo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova atamva fungo labwino anati mu mtima mwake: “Sindidzatembereranso nthaka chifukwa cha munthu, ngakhale kuti maganizo a mu mtima mwake ndi oyipa kuyambira ubwana wake. Ndipo sindidzawononganso zolengedwa zonse zamoyo monga ndachitiramu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anamva conunkhira cakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwace, Sindidzatembereranso konse nthaka cifukwa ca munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu iri yoipa kuyambira pa unyamata wace; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndacitiramo.