Genesis 8:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nthaŵi zonse m'mene dziko lapansi lidzakhalire, padzakhala nyengo yobzala ndi nyengo yokolola. Padzakhala nyengo yachisanu ndi nyengo yotentha, nyengo yachilimwe ndi nyengo yadzinja, ndipo usana ndi usiku zidzakhalapo kosalekeza.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthawi yakubzala ndi yakukunkha, chisanu ndi mafundi, malimwe ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Nthawi zonse mmene dziko lapansi lidzakhalire, nthawi yodzala ndi nthawi yokolola yozizira ndi yotentha, dzinja ndi chilimwe, usana ndi usiku, sizidzatha.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthawi yakubzala ndi yakukunkha, cisanu ndi mafundi, malimwe ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekai.