Genesis 8:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma popeza kuti madzi anali akadalipobe pa dziko lonse, nkhundayo idabwerera, chifukwa idaasoŵa potera. Nowa adatambalitsa dzanja kunja, nailoŵetsanso m'chombo muja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma njiwayo siinapeza popondapo phazi lake, nibwera kwa iye kuchingalawako, pakuti madzi analipo pa dziko lonse lapansi; ndipo anatulutsa dzanja lake, naitenga, nailowetsa kwa iye m'chingalawamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma nkhunda sinapeze poti nʼkutera chifukwa panali madzi ponseponse pa dziko lapansi. Choncho inabwerera kwa Nowa mʼchombo. Nowa anatulutsa dzanja lake kunja ndi kutenga nkhundayo kuyibwezera mʼchombo mmene iye anali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma njiwayo siinapeza popondapo phazi lace, nibwera kwa iye kucingalawako, pakuti madzi analipo pa dziko lonse lapansi; ndipo anaturutsa dzanja lace, naitenga, nailowetsa kwa iye m'cingalawamo.