Genesis 9:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Utawaleza ukamadzaoneka m'mitambo, Ine ndidzaupenya, ndipo ndizidzakumbukira chipangano chamuyaya cha pakati pa Ine ndi zamoyo zonse zokhala pa dziko lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo utawo udzakhala m'mtambo; ndipo ndidzauyang'anira kuti ndikumbukire pangano lachikhalire lili ndi Mulungu ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo pa dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Utawaleza ukamadzaoneka mʼmitambo, ndidzawuona ndi kukumbukira pangano losatha pakati pa Mulungu ndi zamoyo zonse pa dziko lapansi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo utawo udzakhala m'mtambo; ndipo ndidzauyang'anira kuti ndikumbukire pangano lacikhalire liri ndi Mulungu ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo pa dziko lapansi.