Genesis 9:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zamoyo zonse za pa dziko lapansi pamodzi ndi mbalame zomwe, nyama zokwaŵa ndi zonse zam'nyanja zidzakuwopani. Zonsezi ndaziika kuti muzilamule.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuopsa kwanu, ndi kuchititsa mantha kwanu kudzakhala pa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi pa zouluka zonse za m'mlengalenga; ndi pa zonse za m'nyanja, zapatsidwa m'dzanja lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za mlengalenga, ndi chamoyo chilichonse chokwawa, ndiponso nsomba zonse za ku nyanja; zidzakuopani ndipo ndazipereka kuti muzilamulire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kuopsya kwanu, ndi kucititsa mantha kwanu kudzakhala pa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi pa zouluka zonse za m'mlengalenga; ndi pa zonse zokwawa pansi, ndi pa nsomba zonse za m'nyanja, zapatsidwa m'dzanja lanu.