Genesis 9:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Hamu, bambo wake wa Kanani, ataona kuti Nowa bambo wake ali maliseche, adapita nakauza abale ake aŵiri aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Hamu atate wake wa Kanani, anauona umaliseche wa atate wake, nauza abale ake awiri amene anali kunja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hamu, abambo ake a Kanaani ataona kuti abambo ake ali maliseche anakawuza abale ake awiri aja omwe anali panja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Hamu atate wace wa Kanani, anauona umarisece wa atate wace, nauza abale ace awiri amene anali kunja.