Genesis 9:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Semu ndi Yafeti adatenga chofunda nachiika kumbuyo kwao, atachinyamula pa mapewa. Tsono adayenda chafutambuyo nafunditsa bambo wao. Sadapenyeko kumene kunali bambo wao uja ndipo sadaone maliseche ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Semu ndi Yafeti ndipo anatenga chofunda, nachiika pa mapewa ao a onse awiri, nayenda chambuyo, nafunditsa umaliseche wa atate wao: nkhope zao zinali chambuyo, osaona umaliseche wa atate ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Semu ndi Yafeti anatenga chofunda nachiyika pa mapewa awo; ndipo anayenda chamʼmbuyo naphimba umaliseche wa abambo awo. Anafulatira kuti asaone umaliseche wa abambo awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Semu ndi Yafeti ndipo anatenga copfunda, naciika pa mapewa ao a onse awiri, nayenda cambuyo, napfunditsa umarisece wa atate wao: nkhope zao zinali cambuyo, osaona umarisece wa atate ao.