Genesis 9:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Aliyense wopha munthu, nayenso adzaphedwa, pakuti munthu adalengedwa muchifaniziro cha Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa: chifukwa m'chifanizo cha Mulungu Iye anampanga munthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Aliyense wopha munthu, adzaphedwanso ndi munthu; pakuti Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wace udzakhetsedwa: cifukwa m'cifanizo ca Mulungu Iye anampanga munthu.