Habakkuk 1:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta, kodi suja ndinu wachikhalire? Ndinu Mulungu wanga, Woyera wanga uja, wosafa. Inu Chauta, ndinu amene mudaŵasankha anthuwo kuti abweretse chiweruzo pa ife. Inu Thanthwe lathu, mudaŵaika iwowo kuti atilange.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Si ndinu wachikhalire, Yehova Mulungu wanga, wopatulika wanga? Sitidzafa. Yehova munamuikiratu kuti aweruzidwe; ndipo Inu, Thanthwe, munamkhazika kuti alangidwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu Yehova, kodi sindinu wachikhalire? Mulungu wanga, Woyera wanga, ife sitidzafa. Inu Yehova, munawasankha anthuwo kuti abweretse chiweruzo; Inu Thanthwe, munawayika iwowo kuti atilange.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Si ndinu wacikhalire, Yehova Mulungu wanga, wopatulika wanga? sitidzafa. Yehova munamuikiratu kuti aweruzidwe; ndipo Inu, Thanthwe, munamkhazika kuti alangidwe.