Habakkuk 1:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Maso anu ndi oyera, safuna kuwona zoipa, simungalekerere anthu ochita uchimo ndi zolakwa. Chifukwa chiyani nanga mukulekerera anthu osakhulupirikawo? Bwanji simuchitapo kanthu pamene anthu oipa akuwononga anthu abwino kupambana iwowo?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inu wa maso osalakwa, osapenya choipa, osakhoza kupenyerera chovuta, mupenyereranji iwo akuchita mochenjerera, ndi kukhala chete pamene woipa ammeza munthu wolungama woposa iye mwini;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Maso anu ndi oyera kwambiri safuna kuona choyipa; Inu simulekerera cholakwa. Chifukwa chiyani nanga mukulekerera anthu ochita zachinyengowa? Chifukwa chiyani muli chete pamene anthu oyipa akuwononga anthu olungama kupambana iwowo?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inu wa maso osalakwa, osapenya coipa, osakhoza kupenyerera cobvuta, mupenyereranji iwo akucita mocenjerera, ndi kukhala cete pamene woipa ammeza munthu wolungama woposa iye mwini;