Habakkuk 1:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono amaperekera nsembe makombe ao, ndipo amafukizira lubani matchera ao. Chifukwa zimenezi ndizo zimaŵabweretsera moyo wapamwamba, ndipo amadya bwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake aphera nsembe ukonde wake, nafukizira khoka lake, pakuti mwa izi gawo lake lilemera, ndi chakudya chake chichuluka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho iye amaperekera nsembe ukonde wake ndiponso kufukizira lubani khoka lake, popeza ukonde wakewo ndiye umamubweretsera moyo wapamwamba ndipo amadya chakudya chabwino kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace aphera nsembe ukonde wace, nafukizira khoka lace, pakuti mwa izi gawo lace lilemera, ndi cakudya cace cicuruka.