Habakkuk 1:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi Inu Chauta, ndidzakhala ndikukupemphani chithandizo nthaŵi yaitali bwanji, Inuyo osandiyankha? Kapena kukudandaulirani kuti “Nkhondo kuno,” Inuyo osatipulumutsa?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova, ndidzafuula mpaka liti osamva Inu? Ndifuulira kwa Inu za chiwawa, koma simupulumutsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi inu Yehova, ndidzakhala ndikukupemphani thandizo kwa nthawi yayitali motani, koma wosayankha? Kapena kufuwulira kwa inu kuti, “Chiwawa kuno!” koma wosatipulumutsa?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova, ndidzapfuula mpaka liti osamva Inu? ndipfuulira kwa Inu za ciwawa, koma simupulumutsa.