Habakkuk 1:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa chiyani mukufuna kuti ndiziwona mavuto otereŵa. Chifukwa chiyani mukulekerera zoipa? Ponseponse ndikuwona chiwonongeko ndiponso nkhondo. Pali ndeu ndi kukangana kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mundionetseranji zopanda pake, ndi kundionetsa zovuta? Pakuti kufunkha ndi chiwawa zili pamaso panga; ndipo pali ndeu, nauka makani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chiyani mukundionetsa zinthu zoyipa? Chifukwa chiyani mukundionetsa mavutowa? Ndikuona chiwonongeko ndi chiwawa; pali ndewu ndi kukangana kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mundionetseranji zopanda pace, ndi kundionetsa zobvuta? pakuti kufunkha ndi ciwawa ziri pamaso panga; ndipo pali ndeli nauka makani.