Habakkuk 1:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye kuti malamulo atha mphamvu. Chilungamo sichikugwira ntchito. Anthu oipa akupambana anthu abwino, motero chilungamo chalephereka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti chilamulo chalekeka, ndi chiweruzo sichitulukira konse; popeza woipa azinga wolungama, chifukwa chake chiweruzo chituluka chopindika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero malamulo anu atha mphamvu, ndipo chilungamo sichikugwira ntchito. Anthu oyipa aposa olungama, kotero apotoza chilungamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti cilamulo calekeka, ndi ciweruzo siciturukira konse; popeza woipa azinga wolungama, cifukwa cace ciweruzo cituruka copindika.