Habakkuk 1:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye kuti ndidzakweza Ababiloni mtundu woopsa ndi wamphamvu. Iwowo amapita pa dziko lonse lapansi kuti akalande malo a eniake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti taonani, ndiukitsa Ababiloni, mtundu uja wowawa ndi waliwiro, wopitira pa chitando cha dziko lapansi, kulowa m'malo mosati mwao, mukhale mwaomwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti taonani, Ine ndikuwutsa Ababuloni, anthu ankhanza ndiponso amphamvu, amene amapita pa dziko lonse lapansi kukalanda malo amene si awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti taonani, ndiukitsa Akasidi, mtundu uja wowawa ndi waliwiro, wopitira, pa citando ca dziko lapansi, kulowa m'malo mosati mwao, mukhale mwao mwao.