Habakkuk 1:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akavalo ao ndi aliŵiro kwambiri kupambana akambuku, ndi oopsa kupambana mimbulu yolusa. Okwerapo ao akuthamanga molunjika kuchokera kutali. Akuchita kugudukira ngati chiwombankhanga chofuna kugwira nyama.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akavalo ao aposa anyalugwe liwiro lao, aposa mimbulu ya madzulo ukali wao, ndipo apakavalo ao atanda; inde apakavalo ao afumira kutali; auluka ngati chiombankhanga chofulumira kudya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akavalo awo ndi aliwiro kwambiri kupambana akambuku ndi owopsa kupambana mimbulu yolusa nthawi ya madzulo. Okwerapo awo akuthamanga molunjika; a pa akavalo awo ndi ochokera kutali, akuwuluka ngati chiwombankhanga chofuna kugwira nyama;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akavalo ao aposa anyalugwe liwiro lao, aposa mimbulu ya madzulo ukali wao, ndipo apakavalo ao atanda; inde apakavalo ao afumira kutali; auluka ngati ciombankhanga cofulumira kudya.