Habakkuk 2:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakhala ngati mlonda, woimirira pa linga. Ndidzaona zimene adzandiwuze, apo ndidzadziŵa zimene adzayankhe za dandaulo langa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzaima pa dindiro langa ndi kudziika palinga, ndipo ndidzayang'anira ndione ngati adzanenanji mwa ine, ngatinso ndidzamyankha chiyani pa choneneza changa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzakhala pa malo anga aulonda, ndi kuyima pa mitumbira ya nkhondo; ndidzadikira kuti ndimve zimene Iye adzandiwuze, ndi yankho limene ndidzapatsidwe pa madandawulo anga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzaima pa dindiro langa ndi kudziika palinga, ndipo ndidzayang'anira ndione ngati adzanenanji mwa ine, ngatinso ndidzamyankha ciani pa coneneza canga.