Habakkuk 2:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Chauta Wamphamvuzonse ndiye watsimikiza kuti zimene anthu amagwirira ntchito zili ngati nkhuni pa moto. Anthu a mitundu yonse amangodzitopetsa popanda phindu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, sichichokera kwa Yehova wa makamu kodi kuti mitundu ya anthu ingogwirira moto ntchito, ndi anthu angodzilemetsa pa zopanda pake?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi Yehova Wamphamvuzonse sanatsimikize kuti ntchito za anthu zili ngati nkhuni pa moto, ndi kuti mitundu ya anthu imadzitopetsa popanda phindu?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, sicicokera kwa Yehova wa makamu kodi kuti mitundu ya anthu ingogwirira moto nchito, ndi anthu angodzilemetsa pa zopanda pace?