Habakkuk 2:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma amene udzachite manyazi ndiwe ndipo onse adzakunyoza kwambiri. Tsopano imwa ndiwe, mpaka kudzandira. Chikho cha chilango cha Chauta chikupeza, ndipo manyazi adzaphimba ulemerero wako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Udzazidwa nao manyazi m'malo mwa ulemerero; imwa iwenso, nukhale wosadulidwa; chikho cha dzanja lamanja la Yehova chidzatembenukira iwe, ndi kusanza kwa manyazi kudzakhala pa ulemerero wako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Udzachita manyazi mʼmalo mokhala ndi ulemerero. Tsopano ino ndi nthawi yako! Imwa mpaka umaliseche wako uwonekere! Chikho chochokera mʼdzanja lamanja la Yehova chikubwera kwa iwe, ndipo manyazi adzaphimba ulemerero wako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Udzazidwa nao manyazi m'malo mwa ulemerero; imwa iwenso, nukhale wosadulidwa; cikho ca dzanja lamanja la Yehova cidzatembenukira iwe, ndi kusanza kwa manyazi kudzakhala pa ulemerero wako,