Habakkuk 2:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udzachita mantha chifukwa cha kusakaza nkhalango za ku Lebanoni. Udzaopsedwa chifukwa cha kuwononga nyama zake. Wakhetsa magazi a anthu mwankhanza, waononga mizinda ndi onse okhalamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti chiwawa chidachitikira Lebanoni chidzakukuta, ndi chionongeko cha nyama chidzakuopsa; chifukwa cha mwazi wa anthu, ndi chiwawa chochitidwira dziko, mudzi, ndi onse okhalamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Udzathedwa nzeru ndi chiwawa chimene unachita ku Lebanoni, ndiponso udzachita mantha ndi nyama zimene unaziwononga. Pakuti wakhetsa magazi a anthu; wawononga mayiko ndi mizinda ndi aliyense wokhala mʼmenemo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ciwawa cidacitikira Lebano cidzakukuta, ndi cionongeko ca nyama cidzakuopsa; cifukwa ca mwazi wa anthu, ndi ciwawa cocitidwira dziko, mudzi, ndi onseokhalamo.