Habakkuk 2:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsoka kwa amene amauza mtengo kuti, “Nyamuka!” Amene amauza mwala waduu kuti, “Dzuka!” Kodi zimenezi zingathe kulangiza? Nzopangidwa ndi golide ndi siliva, ndipo sizitha konse kupuma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsoka iye wakunena kwa mtengo, Galamuka; ndi kwa mwala wosalankhula, Nyamuka! Kodi ichi chiphunzitsa? Taona chakutidwa ndi golide ndi siliva, ndi m'kati mwake mulibe mpweya konse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsoka kwa amene amawuza mtengo kuti, ‘Khala wamoyo!’ Kapena mwala wopanda moyo kuti, ‘Dzuka!’ Kodi zimenezi zingathe kulangiza? Ndi zokutidwa ndi golide ndi siliva; mʼkati mwake mulibe mpweya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsoka iye wakunena kwa mtengo, Galamuka; ndi kwa mwala wosalankhula, Nyamuka Kodi ici ciphunzitsa? Taona cakutidwa ndi golidi ndi siliva, ndi m'kati mwace mulibe mpweya konse.