Habakkuk 2:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ogwidwawo adzamnyoza, adzamnyodola ponena kuti, “Tsoka kwa amene amadzikundikira chuma chosakhala chake, amene amalemera ndi ngongole zosalungama. Adzatero mpaka liti?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi sadzamnenera fanizo onsewo, ndi mwambi womnyodola, ndi kuti, Tsoka iye wochulukitsa zimene sizili zake? Mpaka liti? Iye wodzisenzera zigwiriro.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kodi onse ogwidwawo sadzamunyoza ndi kumunyogodola ponena kuti, “Tsoka kwa amene amadzikundikira katundu amene si wake ndipo amadzilemeretsa ndi chuma cholanda! Kodi izi zidzachitika mpaka liti?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi sadzamnenera fanizo onsewo, ndi mwambi womnyodola, ndi kuti, Tsoka iye wocurukitsa zimene siziri zace! mpaka liti? iye wodzisenzera zigwiriro.