Habakkuk 2:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa iweyo udafunkha mitundu yambiri ya anthu, koma otsala adzakufunkha iweyo, chifukwa chokhetsa magazi a anthu ambiri, ndiponso chifukwa choononga mwankhanza mizinda ndi onse okhalamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza iwe wafunkha amitundu ambiri, otsala onse a mitundu ya anthu adzakufunkha iwe; chifukwa cha mwazi wa anthu, ndi chiwawa chochitikira dziko, mudzi, ndi onse okhalamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti unafunkha mitundu yambiri ya anthu, mitundu ina imene inatsala idzakufunkha iweyo. Pakuti wakhetsa magazi a anthu; wawononga mayiko ndi mizinda ndi aliyense wokhala mʼmenemo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza iwe wafunkha amitundu ambiri, otsala onse a mitundu ya anthu adzakufunkha iwe; cifukwa ca mwazi wa anthu, ndi ciwawa cocitikira dziko, mudzi, ndi onse okhalamo.