Habakkuk 3:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mapiri atakuwonani adayamba kugwedezeka. Madzi amphamvu am'mitsinje adasefukira. Nyanja yozama idakokoma, mafunde ake adakwera kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mapiri anakuonani, namva zowawa; chigumula cha madzi chinapita; madzi akuya anamveketsa mau ake, nakweza manja ake m'mwamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mapiri anakuonani ndipo anagwedezeka. Madzi amphamvu anasefukira; nyanja yozama inakokoma ndipo mafunde ake anakwera kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mapiri anakuonani, namva zawawa; Cigumula ca madzi cinapita; Madzi akuya anamveketsa mau ace, Nakweza manja ace m'mwamba.