Habakkuk 3:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudapita kukapulumutsa anthu anu, mudabwera kudzalanditsa wodzozedwa wanu. Mudakantha mtsogoleri wa dziko la anthu oipa, mudaonongeratu anthu ake onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munatulukira chipulumutso cha anthu anu, chipulumutso cha odzozedwa anu; munakantha mutu wa nyumba ya woipa, ndi kufukula maziko kufikira m'khosi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munapita kukalanditsa anthu anu, kukapulumutsa wodzozedwa wanu. Munakantha mtsogoleri wa dziko la anthu oyipa, munawononga anthu ake onse. Sela
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munaturukira cipulumutso ca anthu anu, Cipulumutso ca odzozedwa anu; Munakantha mutu wa nyumba yawoipa, Ndi kufukula maziko kufikira m'khosi.