Habakkuk 3:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndi mivi yanu mudalasa mtsogoleri wa ankhondo ake, amene adaabwera ngati kamvulumvulu kuti atibalalitse. Ankakondwerera ngati kuti akudzaononga osauka mwachinsinsi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munapyoza ndi maluti ake mutu wa ankhondo ake; anadza ngati kamvulumvulu kundimwaza; kukondwerera kwao kunanga kufuna kutha ozunzika mobisika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndi mkondo wake womwe munalasa mtsogoleri wake pamene ankhondo ake anabwera mwamphamvu kudzatibalalitsa, ankasangalala ngati kuti akudzawononga osauka amene akubisala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munapyoza ndi maluti ace mutu wa ankhondo ace; Anadza ngati kabvumvulu kundimwaza; Kukondwerera kwao kunanga kufuna kutha ozunzika mabisika.