Habakkuk 3:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Izi ndazimva, ndipo thupi langa likunjenjemera, m'kamwa fuu chifukwa cha phokosolo. M'mafupa mwazizira, ndipo maondo akuwombana. Ndikudikira tsiku la chilango chimene chidzagwera amene akutithira nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinamva, ndi m'mimba mwanga munabwadamuka, milomo yanga inanthunthumira pamau, m'mafupa mwanga mudalowa chivundi, ndipo ndinanjenjemera m'malo mwanga; kuti ndipumule tsiku lamsauko, pamene akwerera anthu kuti ayambane nao ndi makamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinamva ndipo mtima wanga unagunda kwambiri, milomo yanga inanjenjemera pakumva phokosolo; mafupa anga anaguluka, ndipo mawondo anga anawombana. Komabe ndikuyembekezera mofatsa, tsiku la masautso limene lidzafike pa mtundu wa anthu umene ukutithira nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinamva, ndi m'mimba mwanga munabwadamuka, Milomo yanga inanthunthumira pamau, M'mafupa mwanga mudalowa cibvundi, ndipo ndinanjenjemera m'malo mwanga; Kuti ndipumule tsiku lamsauko, Pamene akwerera anthu kuti ayambane nao ndi makamu.