Habakkuk 3:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta, ndamva za mbiri yanu, Inu Chauta, ntchito zanu zandiwopsa. Muzichitenso masiku ano, zikhale zodziŵika makono. Ngakhale muli okwiya, musaiŵale chifundo chanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova, ndinamva mbiri yanu ndi mantha; Yehova, tsitsimutsani ntchito yanu pakati pa zaka, pakati pa zaka mudziwitse; pa mkwiyo mukumbukire chifundo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu Yehova, ndamva za kutchuka kwanu; Inu Yehova, ntchito zanu zandiopsa. Muzichitenso masiku athu ano, masiku athu ano zidziwike; mu ukali wanu mukumbukire kuchita chifundo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova, ndinamva mbiri yanu ndi mantha; Yehova, tsitsimutsani nchito yanu pakati pa zaka, Pakati pa zaka mudziwitse; Pa mkwiyo mukumbukile cifundo.