Habakkuk 3:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaimirira ndipo dziko lapansi lidagwedezeka. Adayang'ana ndipo mitundu ya anthu idanjenjemera. Pomwepo mapiri okhazikika adagumuka, ndipo magomo akalekale adatera, njira zake nzachikhalire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anaimirira, nandengulitsa dziko lapansi; anapenya, nanjenjemeretsa amitundu; ndi mapiri achikhalire anamwazika, zitunda za kale lomwe zinawerama; mayendedwe ake ndiwo a kale lomwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayimirira ndi kugwedeza dziko lapansi; anayangʼana ndipo mitundu ya anthu inanjenjemera. Mapiri okhazikika anagumuka ndipo zitunda zakalekale zinatitimira. Njira zake ndi zachikhalire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anaimirira, nandengulitsa dziko lapansi; Anapenya, nanjenjemeretsa amitundu; Ndi mapiri acikhalire anamwazika, Zitunda za kale lomwe zinawerama; Mayendedwe ace ndiwo a kale lomwe.