Haggai 1:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Zerubabele mwana wa Salatiyele, Yoswa mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe, ndi anthu ena onse obwerako ku ukapolo, adachita zimene Chauta Mulungu wao adanena. Adamva mau a mneneri Hagai amene Chauta adamtuma, ndipo adachita mantha kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi otsala onse a anthu, anamvera mau a Yehova Mulungu wao, ndi mau a Hagai mneneri, monga Yehova Mulungu wao adamtuma; ndipo anthu anaopa pamaso pa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Zerubabeli mwana wa Sealatieli, mkulu wa ansembe Yoswa mwana wa Yehozadaki, ndi anthu onse otsala anamvera mawu a Yehova Mulungu wawo ndi uthenga wa Hagai, chifukwa anatumidwa ndi Yehova Mulungu wawo. Ndipo anthuwo anaopa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealitiyeli, ndi Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkuru wa ansembe, ndi otsala onse a anthu, anamvera mau a Yehova Mulungu wao, ndi mau a Hagai mneneri, monga Yehova Mulungu wao adamtuma; ndipo anthu anaopa pamaso pa Yehova.