Haggai 1:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Hagai, wamthenga uja, adaŵauza mau a Chauta akuti, “Ine Chauta ndikukuuzani kuti ndili nanu ndithu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Hagai mthenga wa Yehova, m'uthenga wa Yehova ananena ndi anthu, ndi kuti, Ine ndili nanu, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Hagai, mthenga wa Yehova, anapereka kwa anthuwo uthenga uwu wa Yehova: “Ine ndili nanu,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Hagai mthenga wa Yehova m'uthenga wa Yehova ananena ndi anthu, ndi kuti, Ine ndiri nanu, ati Yehova.