Haggai 1:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adalimbitsa mtima Zerubabele mwana wa Salatiyele, bwanamkubwa wa ku Yuda, ndi Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndiponso anthu ena onse. Adabwera, nayamba kugwira ntchito yomanga Nyumba ya Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wao,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anautsa mzimu wa Zerubabele mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi mzimu wa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi mzimu wa otsala onse a anthu, ndipo anadza nagwira ntchito m'nyumba ya Yehova wa makamu, Mulungu wao,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero Yehova anakhudza mtima wa Zerubabeli mwana wa Sealatieli, bwanamkubwa wa Yuda, mtima wa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndiponso mitima ya anthu onse otsala. Iwo anabwera ndi kuyamba ntchito yomanga Nyumba ya Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wawo,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anautsa mzimu wa Zerubabele mwana wa Sealitiyeli, ciwanga ca Yuda, ndi mzimu wa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi mzimu wa otsala onse a anthu, ndipo anadza nagwira nchito m'nyumba ya Yehova wa makamu, Mulungu wao,