Haggai 1:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwafesa zambiri, koma mwakolola pang'ono. Mumadya, koma osakhuta. Mumamwa, koma ludzu osatha. Mumavala, koma osamva kufunda. Malipiro a anthu antchito ndi osakwanira mpang'ono pomwe,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwabzala zambiri, koma mututa pang'ono; mukudya, koma osakhuta; mukumwa, koma osakoledwa; mudziveka, koma palibe wofundidwa; ndi iye wolembedwa ntchito yakulipidwa alandirira kulipirako m'thumba lobooka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwadzala zambiri, koma mwakolola zochepa. Mumadya, koma simukhuta. Mumamwa, koma ludzu lanu silitha. Mumavala, koma simumva kutentha. Mumalandira malipiro, koma ndalama zanu zimatha ngati mwaziyika mʼthumba lobowoka.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwabzala zambiri, koma mututa pang'ono; mukudya, koma osakhuta; mukumwa, koma osakoledwa; mudzibveka, koma palibe wofundidwa; ndi iye wolembedwa nchito yakulipidwa alandirira kulipirako m'thumba lobooka.