Haggai 1:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mwakhala mukuyembekeza zokolola zambiri, koma mwangopeza pang'ono. Pamene munkatuta zokolola zanu, Ine ndidangozimwazamwaza. Tsono Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikuti, Ndidachitiranji zimenezi? Chifukwa chake nchakuti Nyumba yanga ndi bwinja, pamene aliyense akutanganidwa nkumanga nyumba yake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munayembekezera zambiri, koma taonani, pang'ono; ndipo, mutabwera napo kwanu, ndinauzirapo. Chifukwa ninji? Ati Yehova wa makamu. Chifukwa cha nyumba yanga yokhala yopasuka, ndipo nuthamangira yense kunyumba kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mumayembekezera zambiri, koma taonani mwapeza pangʼono pokha. Zimene munazibweretsa ku nyumba, Ine ndinazimwaza. Nʼchifukwa chiyani?” Akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Chifukwa Nyumba yanga ikanali bwinja, pamene aliyense wa inu watanganidwa kumanga nyumba yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munayembekezera zambiri, koma taonani, pang'ono; ndipo, mutabwera napo kwanu, ndinauzirapo. Cifukwa ninji? ati Yehova wa makamu. Cifukwa ca nyumba yanga yokhala yopasuka, ndipo nuthamangira yense kunyumba kwace.