Haggai 2:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati munthu wakulunga nyama yopatulika mu mkanjo wake, ndipo mkanjowo ukhudza buledi kapena msuzi, kapena vinyo, kapena mafuta, kapena chakudya cha mtundu wina uliwonse, kodi zimenezinso zidzasanduka zopatulika? Ansembewo adayankha kuti, ‘Iyai.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu akanyamulira nyama yopatulika m'ngudulira, nakhudza mkate, kapena ndiwo, kapena vinyo, kapena mafuta, kapena chakudya chilichonse, ndi ngudulira, kodi chisandulika chopatulika? Ndipo ansembe anayankha nati, Iai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati munthu wakulunga nyama yopatulika mu mkanjo wake, ndipo mkanjowo nʼkukhudza buledi kapena msuzi, kapena vinyo, mafuta kapena chakudya cha mtundu wina uliwonse, kodi zimenezo zimasanduka zopatulika?’ ” Ansembe anayankha kuti, “Ayi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu akanyamulira nyama yopatulika m'ngudulira, nakhudza mkate, kapena ndiwo, kapena vinyo, kapena mafuta, kapena cakudya ciri conse, ndi ngudulira, kodi cisandulika copatulika? Ndipo ansembe anayankha nati, Iai.