Haggai 2:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Hagai adaŵafunsanso kuti, “Nanga ngati munthu amene adaipitsidwa pokhudza mtembo, akhudzanso zimenezi, ndiye kuti zimenezinso zidzaipitsidwa?” Ansembe adayankha kuti, “Inde, zidzaipitsidwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Hagai anati, Munthu wodetsedwa ndi mtembo akakhudza kanthu ka izi, kodi kali kodetsedwa kanthuka? Ndipo ansembe anayankha nati, Kadzakhala kodetsedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Hagai anati, “Ngati munthu amene anayipitsidwa pokhudza mtembo akhudza chimodzi cha zinthu zimenezi, kodi chinthucho chimayipitsidwa?” Ansembe anayankha kuti, “Inde, chimayipitsidwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Hagai anati, Munthu wodetsedwa ndi mtembo akakhudza kanthu ka izi, kodi kali kodetsedwa kanthuka? Ndipo ansembe anayankha nati, Kadzakhala kodetsedwa.