Haggai 2:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Hagai adanena kuti, “Zimene akunena Chauta ndi izi: ‘Nchimodzimodzinso ndi anthu ameneŵa, nchimodzimodzinso ndi mtundu umenewu pamaso panga. Zonse zimene amachita ndi zonse zimene amapereka ku nsembe nzoipitsidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Hagai anayankha, nati, Momwemo anthu awa, ndi momwemo mtundu uwu pamaso panga, ati Yehova; ndi momwemo ntchito iliyonse ya manja ao; ndi ichi achipereka, chili chodetsedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Hagai anati, “ ‘Ndi mmene zilili ndi anthu awa ndi dziko ili pamaso panga,’ akutero Yehova. ‘Chilichonse amachita ndiponso chilichonse chimene amapereka nʼchodetsedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Hagai anayankha, nati, Momwemo anthu awa, ndi momwemo mtundu uwu pamaso panga, ati Yehova; ndi momwemo nchito iri yonse ya manja ao; ndi ici acipereka, ciri codetsedwa.