Haggai 2:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene munthu ankayembekeza kupeza miyeso ya tirigu makumi aŵiri ankangopeza khumi yokha. Akabwera kuti adzatunge miyeso makumi asanu mu mtsuko wa vinyo, ankangopeza makumi aŵiri okha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo ponse munthu akadza ku mulu woyenera miyeso makumi awiri, pali khumi yokha; munthu akadza ku choponderamo mphesa kudzatunga mbiya makumi asanu, pali makumi awiri okha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene munthu ankayembekezera miyeso ya tirigu makumi awiri ankangopeza khumi yokha. Munthu akapita kuti akatunge miyeso makumi asanu ya vinyo mu mtsuko, ankangopeza miyeso makumi awiri yokha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo ponse munthu akadza ku mulu woyenera miyeso makumi awiri, pali khumi yokha; munthu akadza ku coponderamo mphesa kudzatunga mbiya makumi asanu, pali makumi awiri okha.