Haggai 2:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzagwetsa mafumu a mitundu ya anthu akunja ndi kuwononga mphamvu za maufumu ao. Ndidzagubuduza magaleta ndi okwerapo ake. Akavalo adzafa, ndipo okwerapo ao adzaphana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndidzagubuduza mipando yachifumu ya maufumu, ndidzaononga mphamvu ya maufumu a amitundu; ndidzagubuduza magaleta ndi iwo akuyendapo; ndi akavalo ndi apakavalo adzatsika, yense ndi lupanga la mbale wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzagwetsa mipando yaufumu ndi kuwononga mphamvu za maufumu achilendo. Ndidzagubuduza magaleta ndi okwerapo ake; akavalo ndi okwerapo ake adzagwa, aliyense adzaphedwa ndi lupanga la mʼbale wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndidzagubuduza mipando yacifumu ya maufumu, ndidzaononga mphamvu ya maufumu a amitundu; ndidzagubuduza magareta ndi iwo akuyendapo; ndi akavalo ndi apakavalo adzatsika, yense ndi lupanga la mbale wace.