Haggai 2:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ine Chauta Wamphamvuzonse mau anga ndi aŵa: Pa tsiku limenelo iwe Zerubabele mtumiki wanga, mwana wa Salatiyele, ndidzakutenga ndipo ndidzakusandutsa wolamulira m'dzina langa, pakuti ndiwe amene ndakusankhula. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzakutenga, Zerubabele mtumiki wanga, mwana wa Sealatiele, ati Yehova, ndi kuika iwe ngati mphete yosindikizira; pakuti ndakusankha, ati Yehova wa makamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Tsiku limenelo,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse, ‘ndidzakutenga, iwe mtumiki wanga Zerubabeli mwana wa Sealatieli,’ akutero Yehova, ‘ndipo ndidzakusandutsa kukhala mphete yanga yolamulira, pakuti ndasankha iwe,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzakutenga, Zerubabele mtumiki wanga, mwana wa Sealitiyeli, ati Yehova, ndi kuika iwe ngati mphete yosindikizira; pakuti ndakusankha, ati Yehova wa makamu.