Haggai 2:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kodi alipo ena mwa inu amene adaaona ulemerero wakale wa Nyumba iyi? Monga simukuwona kuti tsopano ulemererowo watheratu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adatsala ndani mwa inu amene anaona nyumba iyi m'ulemerero wake woyamba? Ndipo muiona yotani tsopano? Kodi siikhala m'maso mwanu ngati chabe?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
‘Kodi alipo amene watsala pakati panu amene anaona ulemerero wakale wa Nyumba iyi? Nanga tsopano ikuoneka motani kwa inu? Kodi sikuoneka ngati yopanda pake kwa inu?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adatsala ndani mwa inu amene anaona nyumba iyi m'ulemerero wace woyamba? ndipo muiona yotani tsopano? Kodi siikhala m'maso mwanu ngati cabe?