Haggai 2:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikuti, usataye mtima iwe Zerubabele, usataye mtima iwe Yoswa, mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, musataye mtima inu nonse. Yambani ntchito, pakuti Ine ndili nanu ndithu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma limbika tsopano, Zerubabele, ati Yehova; ulimbikenso Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe; ndipo mulimbike inu nonse anthu a m'dziko, ati Yehova, ndi kuchita; pakuti Ine ndili pamodzi ndi inu, ati Yehova wa makamu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe Zerubabeli, limba mtima tsopano,’ akutero Yehova. ‘Limba mtima, iwe Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe. Limbani mtima, anthu nonse a mʼdziko,’ akutero Yehova, ‘ndipo gwirani ntchito. Pakuti ine ndili nanu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma limbika tsopano, Zerubabele, ati Yehova; ulimbikenso Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkuru wa ansembe; ndipo mulimbike inu nonse anthu a m'dziko, ati Yehova, ndi kucita; pakui. Ine ndiri pamodzi ndi inu, ati Yehova wa makamu;