Hebrews 1:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye ndiye kuŵala koonetsa ulemerero wa Mulungu, ndipo ndiye chithunzi chenicheni chosonyeza khalidwe la Mulungu. Iyeyu amachirikiza zonse ndi mau ake amphamvu. Atayeretsa mtundu wa anthu pakuŵachotsa machimo, adakakhala Kumwamba, ku dzanja lamanja la Mulungu waulemerero.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m'mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala pa dzanja lamanja la Ukulu m'Mwamba,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwanayo ndiye kuwala kwa ulemerero wa Mulungu, chithunzithunzi chenicheni cha khalidwe lake. Iyeyu amachirikiza zinthu zonse ndi mphamvu ya mawu ake. Iye atayeretsa anthu kuchoka ku machimo awo, anakhala pansi kumwamba kudzanja lamanja la Mulungu waulemerero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ameneyo, pokhala ali cinyezimiro ca ulemerero wace, ndi cizindikilo ceni ceni ca cikhalidwe cace, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yace, m'mene adacita ciyeretso ca zoipa, anakhala pa dzanja lamanja la Ukulu m'Mwamba,